NEEF Yapempha Alimi Ku Dowa Kukumbukila Kubweza Ngongole

Bungwe lomwe limagawa ngongole kwa anthu mdziko muno la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lapempha alimi komaso anthu omwe akutenga ngongole kuti azikumbukila kubweza pofuna kupititsa patsogolo chitukuko mdziko muno.

Izi zanenedwa pamene bungweli limagawa ngongole ya zipangizo zochitila ulimi wanthilila mudzi mwa Matekenya, mfumu yaikulu Msakambewa m’boma la Dowa.

Malingana ndi mkulu ogwila ntchito kubungweli, a Amos Phiri, alimi omwe alandila zipangizozi akuyenera kulimbikila ulimi wawo kuti asazavutike kubweza ngongole.

Polankhulapo pa mwambowu nduna ya zaulimi a Sam Kawale , ati boma la a Chakwera likuyesetsa kutukula alimi ang’onoang’ono pofuna kukwanilitsa masomphenya a 2063 ofuna kuonetsetsa kuti anthu mdziko muno ali ndi chakudya chokwanila.

“tikamaliza dongosolo lalero a NEEF akhala akuyendabe maderamu pofuna kupeza alimi ena oti awathandize kupeza nawo ngongole imeneyi, Kamba koti masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino ndi ofuna kuonetsatsa kuti wina aliyese asafe ndi njala koma akhale ndi kuthekera kopeza mbewu komaso feteza okwanila” iwo adatero.

Bungwe la NEEF lagawa matumba oposera 800 a feteleza, mbewu,komaso ma pump a solar owathandizila anthu mu ulimi wanthilira.

Wolemba: Sheila Kathewera

Related posts

MRA Urges Journalist to Champion Msonkho Online Awareness

Chakwera Commends Bakhresa Malawi Limited

NLGFC Applauds E-payment in Dowa