Tisadikile Munthu Kuti Afe Kenako Mugula Bokosi

Yemwe akuimila chipani cha MCP pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo mdela la pakati cha kum’mawa kwa boma la Dowa a Martin Luka atsindika zakudzipeleka kwawo pa ntchito yopeleka chinthandizo cha za umoyo kwa anthu okhala ku madela akumidzi.

Iwo alankhula izi mudzi mwa mitembo komwe anapangitsa nsonkhano kutsatila masewero a mpila wa miyendo omwe achinyamata achipanichi anakonza.

A Luka atsindika kuti munthu kuti akavote ayenela kukhala wa nthanzi kotelo sachiona choyenera kuti munthu mudzimuona akufa kenako ndikumangulira bokosi.

“ine si phungu omadikila anthu kuti amwalire kenako ndikumagula mabokosi pomwe kuthekera kopulumutsa miyoyo yawo munali nako ndichifukwa chake ine ndimasamala za umoyo wa anthu a m’dera langa powapatsa thandizo la zaumoyo labwino,” a Luka atero.

Iwo alonjezanso kuti adzakhazikitsa malo omwe achinyamata azikaphunzirako maluso a ntchito za manja monga kuotchelera, kusoka, kukonza galimoto ndi Zina zambiri.

Wapampando wa achinyama a Dickson Ng’oma limbikitsa anthu bomali kuti asakopeke ndi ndalama za ena koma mfundo za chitukuko zomwe zili ndi a Martin Luka.

“Akabwela ndi ndalama zawo adyeleni koma voti yanu kampatseni Martin Luka,” iwo anafotokoza.

Related posts

Halima Daudi Delivers on Campaign Promises

Phungu Wopanda Chipani Alingati Maliro Opanda Mpingo

DEST Members Challenged to Uphold integrity Ahead of September Polls