Ulova ndi Omwe Wavuta

Khwimbi la anthu lasokhana pabwalo la zamasewero la sukulu ya sekondale ya Robert Blake kudzachita nawo mayeso a alangizi a za umoyo (Health Surveillance Assistant) m’boma la Dowa.

Wailesi ya Yetu yapeza kuti aliyense yemwe anakhoza maphunziro a masamu ndi biology ndi credit pa satifiketi ya MSCE ndiomwe akuloledwa kudzalemba mayesowa angakhale kuti maina awo sanapezeke pa ndandanda omwe unatulutsidwa poyamba.

Polankhula wailesi ya Yetu modzi mwa omwe akudzalemba nawo mayesowa a Jailosi Mhango ati iwo akozekera bwino ndipo alindichiyembekezo kuti akhonza mayesowa.

Angakhale zili chomwechi a Mhango apempha adindo kuti achite zinthu mwachilungamo pakasankhidwe ka anthu omwe akhoze mayesowa ponena kuti zizathandizira kupititsa patsogolo ntchito za umoyo m’bomalo akatenga anthu oyenelera.

Related posts

Ministry of Gender, Children, Disability and Social Welfare to increase the number of beneficiaries of Social cash transfer in Dowa

Vocational skills a drive of national development

Trustees of Agriculture Promotion Program TAPP donates maize sheller to Tidziwane Village and Savings Loan Association