Kusintha Ulimi Kukhala Malonda

Nduna ya zaulimi a Sam Dalitso Kawale ati ndi okhutira ndi momwe ntchito ya ulimi wa minda ikukuikulu (Mega Farm) ikuyendera m’boma la Dowa.

A Kawale alankhula izi atamaliza kuyendera minda ikukuikulu ya Lonjezo komanso Bowe EPA ku Mponela m’bomali.

Polankhula ndi wailesi ya Yetu, a Kawale ati ntchito yomwe alimi akuluakulu akugwira m’bomali ikugwirizana ndi masomphenya a boma opanga ulimi kukhala malonda.

A Kawale anaonjeranso kuti chimangachi chithandiziranso maanja a m’bomali kukhala odzidalira pa chakudya.

Kumbali yake, m’modzi mwa alimi omwe amayang’anira munda wa Lonjezo womwe ndi wa mahekitala okwana 82, a Gift Kadam’manja, athokoza boma kamba ka thandizo la zipangizo za ulimi.

A Kadamanja ati akolola matumba achimanga oposera 8000 zomwe paokha sakanakwanitsa.

Pomwe a Wilson Zimba ochokera ku Bowe EPA m’mudzi mwa Chakhadza akuyembekezera kukolora matumba a chimanga opitilira 10,000 pamunda wa mahekitala okwana 112.

Related posts

NEEF Yapempha Alimi Ku Dowa Kukumbukila Kubweza Ngongole

MRA Urges Journalist to Champion Msonkho Online Awareness

Chakwera Commends Bakhresa Malawi Limited