Nduna ya zaulimi a Sam Dalitso Kawale ati ndi okhutira ndi momwe ntchito ya ulimi wa minda ikukuikulu (Mega Farm) ikuyendera m’boma la Dowa.
A Kawale alankhula izi atamaliza kuyendera minda ikukuikulu ya Lonjezo komanso Bowe EPA ku Mponela m’bomali.
Polankhula ndi wailesi ya Yetu, a Kawale ati ntchito yomwe alimi akuluakulu akugwira m’bomali ikugwirizana ndi masomphenya a boma opanga ulimi kukhala malonda.
A Kawale anaonjeranso kuti chimangachi chithandiziranso maanja a m’bomali kukhala odzidalira pa chakudya.
Kumbali yake, m’modzi mwa alimi omwe amayang’anira munda wa Lonjezo womwe ndi wa mahekitala okwana 82, a Gift Kadam’manja, athokoza boma kamba ka thandizo la zipangizo za ulimi.
A Kadamanja ati akolola matumba achimanga oposera 8000 zomwe paokha sakanakwanitsa.
Pomwe a Wilson Zimba ochokera ku Bowe EPA m’mudzi mwa Chakhadza akuyembekezera kukolora matumba a chimanga opitilira 10,000 pamunda wa mahekitala okwana 112.