Phungu Wopanda Chipani Alingati Maliro Opanda Mpingo

Mlembi wa mkulu wa chipani cha Malawi Congress yemwenso ndi nduna ya maboma ang’ono ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe a Richard Chimwendo Banda afanizila aphungu oima pa okha ngati maliro opanda mpingo.

Iwo alankhula izi pa bwalo la zamasewero la Gawamadzi mfumu yaikulu Chiwere pa msonkhano wa ndale m’boma la Dowa.

A Chimwendo ati ndikovuta kukhulupilira munthu yemwe alibe chipani ponena kuti ali ndikuthekera kodzawathawa anthu akadzapambana chisankho.

Iwo apempha anthu m’bomali kuti asadzachite chibwana kusankha munthu yemwe siwachipani cha MCP koma adzasankhe a Martin Luka kamba koti ndi munthu wa khalidwe.

Pa Msonkhanowu phungu yemwe akuimila chipani cha MCP m’dera la pakati kum’mawa kwa boma la Dowa a Martin Luka akhazikitsa mpikisano wa masewero a mpira wa ndalama zokwana K2 million.

Related posts

Halima Daudi Delivers on Campaign Promises

Tisadikile Munthu Kuti Afe Kenako Mugula Bokosi

DEST Members Challenged to Uphold integrity Ahead of September Polls